Chichewa

Amapita kukagula zomwera tiyi

Listen to this article

Kukumana kwanga ndi mkazi wanga kudali koseketsa kwambiri chifukwa ndidakuna naye akupita kukagula shuga ku golosale komanso zomwera tiyi,” adalongosola Fila Ambali.

Nthawi idali itangodutsa 9 koloko m’mawa m’chaka cha 2007 ku Area 47 mu mzinda wa Lilongwe pamene Ambali yemwe amadziwika ndi dzina loti Boss Black, adamuona ndi mkazi wake Fainess George.

Panthawi yomwe Ambali adamuona George mtima wake sudali m’malo. China chake chidamuuza kuti akayese mwayi wake. Mwamphamvu ya Mulungu, zokhumba zake zidatheka.

Fila Ambali, mkazi wake Fainess ndi ana awo

“Komanso chomwe chinandichitisa kuti ndifunsire Fainesi ndi mawonekedwe ake abwino, ayi osanama mwana mkazi amaoneka bwino kwambiri ali mbee, bere lili njoo! Sindidaugwire mtima, koma kutsitsa mfundo zotchakuka.

“Ndidamuuza mbalume zowirira monga munthu wa bambo ukaona chinthu chabwino sufuna kugonja, koma mwatsoka sadandivomere nthawi yomweyo. Padadutsa sabata ziwiri kuti andilole,” adatero Ambali.

Malinga ndi Ambali, sichidali chapafupi kuti amuvomere, komabe zidatheka.

Atatha miyezi isanu ali pachibwenzi, adapanga dongosolo loti mbali zonse ziwiri zikumane asadatengane ngati banja.

Ukwati wawo adadalitsa pa May 6 2015 ku Lansdowne Civic Hall m’dziko la South Africa.

Pofika chaka chino, awiriwo atha zaka 13 ali pa banja.

“Banja lathuli takumana ndi zabwino, komanso zokoma zambiri koma mwachisomo cha Mulungu takhala pa banja za zaka 13 tsopano,” iwo adalongosola.

Iwo adati pomwe pali zabwino, Satana naye amabwera pompo ndikumanga chisa chake ndicholinga chofuna kusokoneza.

Ambali amagwira ntchito yoimba, komanso yogulitsa katundu pa kampani ina m’dziko la South Africa pamene mkazi wake ndi mphunzitsi wa sukulu ya mkombaphala.

Pakadali pano awiriwo akukhalira ku Cape Town m’dziko la South Africa.

Ambali amachokera kwa Chowe m’boma la Mangochi ndipo George amachokera

m’mudzi mwa Maso m’dera la Mfumu kadewere m’boma la Chiradzulu.

Awiriwo akuti mavuto omwe amakumana nawo amathana nawo pokambirana ndi kumvetsetsana.

Related Articles

Back to top button